Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera.
2 Samueli 10:17 - Buku Lopatulika Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani, nakafika ku Helamu. Apo Asiriya adandanda kuti alimbane ndi Davide, ndipo adamenyana nayedi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani ndipo anapita ku Helamu. Aaramu anayima mʼmizere yawo yankhondo kukakumana ndi Davide ndipo anamenyana naye. |
Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera.
Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; Davide naphapo Aaramu apamagaleta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.
Ndipo anamuuza Davide; namemeza iye Aisraele onse, naoloka Yordani, nawadzera, nanika nkhondo ayambane nao. Atandandalitsa nkhondo Davide kuyambana ndi Aaramu, anaponyana naye.