Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.
2 Samueli 1:5 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adamufunsa mnyamatayo kuti, “Iwe wadziŵa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani nawonso adafa?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa nkhaniyi, “Ukudziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?” |
Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.
Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.
Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu; koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu.