pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.
2 Samueli 1:3 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adamufunsa kuti, “Ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndathaŵa ku zithando zankhondo za Aisraele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.” |
pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.
Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.
Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?
Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? Ufumira kuti? Nati iye, Ndili mnyamata wa ku Ejipito, kapolo wa Mwamaleke; mbuye wanga anandisiya, chifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.