Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;
2 Akorinto 3:4 - Buku Lopatulika Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu akudziŵa kuti tikunena zimenezi chifukwa Khristu ndiye amatipatsa kulimba mtima kotere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu. |
Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;
Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.
amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati mu Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu.