2 Akorinto 2:5 - Buku Lopatulika Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititse chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititsa chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati wina aliyense adachita kanthu kolasa mtima, si ineyo amene adalasa mtima, koma pang'ono ponse adalasako nonsenu, kunenatu mosakulitsa nkhani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati wina wamvetsa chisoni, sanamvetse chisoni ine ndekha, koma koposa mosawonjezera wakhumudwitsa nonsenu, kunenatu mosawonjezera. |
Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndili monga inu. Simunandichitire choipa ine;
Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake.