Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.
2 Akorinto 10:16 - Buku Lopatulika kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake tingathe kukubzolani nkukalalika Uthenga Wabwino ku maiko enanso, osanyadira ntchito imene munthu wina wachita kale m'dera lake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti tikalalikire Uthenga Wabwino mu zigawo zina kupitirira kwanuko. Pakuti sitikufuna kudzitama pa ntchito yogwira ena kale mʼdera la munthu wina. |
Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.
ndipo chotero ndinachiyesa chinthu chaulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pamalopo Khristu asanatchulidwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.
Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?