mutafika m'mzinda, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi ino mudzampeza.
1 Samueli 9:14 - Buku Lopatulika Ndipo iwowa anakwera kumzinda; ndipo m'mene analowa m'mzindamo, onani, Samuele anatulukira pali iwo, kuti akakwere kumsanje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwowa anakwera kumudzi; ndipo m'mene analowa m'mudzimo, onani, Samuele anatulukira pali iwo, kuti akakwere kumsanje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adapita kumzindako. Poloŵa mumzindamo, adaona Samuele akutuluka kumene, alikudza kwa iwo pa njira yopita kukachisi kuja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anapita ku mzinda kuja. Akulowa mu mzindamo, anaona Samueli akutuluka mu mzindamo akubwera kumene kunali iwo, koma amapita ku phiri, ku malo wopatulika. |
mutafika m'mzinda, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi ino mudzampeza.
Ndipo Yehova anaululiratu m'khutu la Samuele dzulo lake la tsiku limene Saulo anabwera, kuti,