Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.
1 Samueli 8:21 - Buku Lopatulika Ndipo Samuele anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m'makutu a Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Samuele anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m'makutu a Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Samuele atamva mau onse a anthuwo, adakakambira Chauta mau onsewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli atamva zonse zimene anthuwo ananena, iye anakazifotokozanso kwa Yehova. |
Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.
Pamenepo Yefita anamuka ndi akulu a Giliyadi, ndipo anthu anamuika mkulu wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ake onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.
Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumzinda wake.