idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.
1 Samueli 8:13 - Buku Lopatulika Ndipo idzatenga ana anu aakazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo idzatenga ana anu akazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Izidzatenga ana anu aakazi kuti azidzayenga mafuta onunkhira, ndi kumaphika chakudya ndi kumapanga buledi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyo idzatenga ana anu akazi kuti akhale oyenga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi kupanga buledi. |
idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.
Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mpesa yanu, ndi minda ya azitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake.