Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.
1 Samueli 6:7 - Buku Lopatulika Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye inu, konzani galeta latsopano ndipo mutenge ng'ombe ziŵiri zazikazi zamkaka zimene sizidavalepo goli ndi kale lonse. Mumange ng'ombezo ku galeta, koma makonyani ake muŵasiye kumudzi kwanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu. |
Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.
Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa galeta watsopano kuchokera kunyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa galetayo.
Ili ndi lemba la chilamulo Yehova adalamulirachi, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele kuti azikutengera ng'ombe yaikazi yofiira, yangwiro yopanda chilema, yosamanga m'goli;
ndipo kudzali kuti mzinda wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akulu a mzinda uwu atenge ng'ombe yaikazi yosagwira ntchito, yosakoka goli;
ndipo akulu a mzinda uwu atsike nayo ng'ombeyo ku chigwa choyendako madzi, chosalima ndi chosabzala, nayidula khosi ng'ombeyo m'chigwamo;