Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 13:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa galeta watsopano kuchokera kunyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa galetayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa galeta watsopano kuchokera kunyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa galetayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Bokosi lachipanganolo adalinyamula pa ngolo yatsopano, kuchoka nalo ku nyumba ya Abinadabu. Uza ndi Ahiyo ndiwo amene ankayendetsa ngoloyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iwo anachotsa Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu pa ngolo yatsopano. Uza ndi Ahiyo ndiwo ankayendetsa ngoloyo.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 13:7
7 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.


Potuluka nalo tsono pamodzi ndi likasa la Mulungu m'nyumba ya Abinadabu ili pachitunda, Ahiyo anatsogolera likasalo.


Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.


Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha.


Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.


Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa