Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
1 Samueli 4:19 - Buku Lopatulika Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵiyo mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali ndi pathupi ndipo anali pafupi kuchira. Pamene adamva zakuti Bokosi lachipangano la Chauta lidalandidwa, ndiponso kuti Eli, mpongozi wake, pamodzi ndi mwamuna wake adafa, zoŵaŵa za pobala mwana zidamfikira mwadzidzidzi, mwana nkumabadwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawiyo, mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali woyembekezera ndipo anali pafupi kuchira. Atamva kuti Bokosi la Mulungu lalandidwa ndi kuti mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake amwalira, ululu wa pobereka mwana unamufikira modzidzimutsa ndipo anabereka mwana. |
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Ndipo panali pamene anavutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna.
pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.
Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai.
Ndipo pamene adati amwalire, anthu aakazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira.