Yeremiya 26:6 - Buku Lopatulika6 pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mudzi uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 ndiye kuti Nyumba ino ndidzaiwononga monga m'mene ndidaonongera Silo. Ndipo mzinda uno ndidzausandutsa chinthu chonyozeka kwa mitundu yonse ya pa dziko lapansi!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ” Onani mutuwo |
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.