Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake?
1 Samueli 3:10 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthaŵi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “Lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!” Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.” |
Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake?
Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga aamuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva.
Ndipo Samuele anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.
Ndipo Yehova anaonekanso mu Silo, pakuti Yehova anadziwulula kwa Samuele ku Silo, mwa mau a Yehova.
Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.
Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m'malo mwake.