Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
1 Samueli 26:5 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye Davide adanyamuka nakafika pa malo amene Saulo adaamangapo zithando zake. Ndipo adaona malo amene ankagonapo Sauloyo ndi Abinere mwana wa Nere, mkulu wa ankhondo a Saulo. Sauloyo ankagona m'zithandomo, ndipo gulu lonse lankhondo lidaamanga zithando pomzungulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Davide ananyamuka napita kumalo kumene Sauli anamanga misasa. Iye anaona pamene Sauli ndi Abineri mwana wa Neri mkulu wa ankhondo anagona. Sauli anagona mʼkati mwa tenti ndipo asilikali anagona momuzungulira. |
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.
Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula.
Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.
Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.