Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 26:13 - Buku Lopatulika

Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba paphiri; pakati pao panali danga lalikulu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Davide anaolokera pa phiri; pakati pao panali danga lalikulu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pambuyo pake Davide anadutsa nakakwerera mbali ina ya phiri, ndi kuyimirira pamwamba pa phiri patali. Pakati pawo panali mpata waukulu.

Onani mutuwo



1 Samueli 26:13
4 Mawu Ofanana  

Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu paphiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.


Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.


Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse.


ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?