Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.
1 Samueli 20:4 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Chilichonse mtima wako, unena ndidzakuchitira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Chilichonse mtima wako, unena ndidzakuchitira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yonatani adauza Davide kuti, “Chilichonse chimene unene, ndidzakuchitira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anawuza Davide kuti, “Chilichonse chimene iwe ukufuna kuti ndichite, ndidzakuchitira.” |
Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.
Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake.