Tsono Davide anati kwa Yonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa?
1 Samueli 20:11 - Buku Lopatulika Nati Yonatani kwa Davide, Tiyeni timuke kuthengo. Namuka onse awiri kuthengoko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati Yonatani kwa Davide, Tiyeni timuke kuthengo. Namuka onse awiri kuthengoko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yonatani adayankha kuti, “Tiye tikayende chakumindaku.” Choncho onse aŵiriwo adapita kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anawuza Davide kuti, “Tiyeni tikayende ku mundako.” Ndipo anapita onse awiri. |
Tsono Davide anati kwa Yonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa?
Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi?