Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yopalamula, ndi nsembe yauchimo; kumenenso aziotcha mikate ya ufa wa nsembe, kuti asatuluke nazo kubwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu.
1 Samueli 2:13 - Buku Lopatulika Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sankasamalanso za khalidwe loyenera ansembe pakati pa anthu. Ankachita motere: pamene munthu wina ankapereka nsembe, nyama ilikuŵira pa moto, mtumiki wake wa wansembe ankabwera, atatenga chiforoko cha mano atatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo chizolowezi cha ansembe pakati pa anthu chinali motere kuti pamene munthu aliyense ankapereka nsembe ndipo nyama ija ikuwira pa moto, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi chifoloko cha mano atatu mʼdzanja lake. |
Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yopalamula, ndi nsembe yauchimo; kumenenso aziotcha mikate ya ufa wa nsembe, kuti asatuluke nazo kubwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu.
nachipisa m'chimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene chovuuliracho chinaitulutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yake. Ankatero ku Silo ndi Aisraele onse akufika kumeneko.
Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako.
Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga?