Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.
1 Samueli 17:5 - Buku Lopatulika Ndipo anali ndi chisoti chamkuwa pamutu pake, navala malaya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anali ndi chisoti chamkuwa pamutu pake, navala malaya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ankavala chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo, amene kulemera kwake kunali ngati makilogramu 57. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye ankavala chipewa chamkuwa ndi malaya achitsulo olemera makilogalamu 57. |
Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.
Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.
nakuta msongolo wake ndi chovala chamkuwa, ndiponso pachikota pake panali nthungo yamkuwa.