Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lake kuloza mzinda.
1 Samueli 17:41 - Buku Lopatulika Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula chikopa chake anamtsogolera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula chikopa chake anamtsogolera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mfilistiyo adayambapo kupita kumene kunali Davide, munthu wonyamula chishango ali patsogolo pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mfilisiti uja anayambapo kupita kumene kunali Davide, mnyamata wonyamula zida zake za nkhondo ali patsogolo pake. |
Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lake kuloza mzinda.
Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.
Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.
Ndipo mtengo wa mkondo wake unali ngati mtanda woombera nsalu; ndi mutu wa mkondowo unalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a chitsulo; ndipo womnyamulira chikopa anamtsogolera.