Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, wanthetemyayo ali chiimbire, dzanja la Yehova linamgwera.
1 Samueli 16:23 - Buku Lopatulika Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono nthaŵi zonse mzimu woipa uja ukamfikira Saulo, Davide ankatenga zeze namamuimba. Motero Saulo ankapeza bwino, ndipo mzimu woipawo unkamsiya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi zonse mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu umati ukamufikira Sauli, Davide ankatenga zeze wake nʼkumamuyimbira. Choncho Sauli ankapeza bwino, ndipo mzimu woyipa uja unkamusiya. |
Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, wanthetemyayo ali chiimbire, dzanja la Yehova linamgwera.
Ndipo Saulo anatumiza kwa Yese, nati, Ulole kuti Davide aime pamaso panga; pakuti ndamkomera mtima.