1 Samueli 14:4 - Buku Lopatulika Ndipo pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali ina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzake; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzake ndilo Sene. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali ina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzake; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzake ndilo Sene. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pampata pamene Yonatani ankafuna kudzerapo kuti akafike ku kaboma kankhondo kaja, panali thanthwe lotsetsereka mbali ina, ndi lina lotsetsereka mbali inanso. Dzina la thanthwe lina ankati Bozezi, ndipo linalo ankati Sene. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa mpata pamene Yonatani ankafuna kudutsa kukafika ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti kunali thanthwe lotsetsereka mbali ina ndi lina lotsetsereka mbali inayo. Thanthwe limodzi linkatchedwa Bozezi ndipo linalo linkatchedwa Seni. |
Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzake kumwera pandunji pa Geba.