Chomwecho Amasa anamuka kukaitana anthu a Yuda asonkhane; koma anachedwa, napitiriza nthawi imene idamuikira.
1 Samueli 13:8 - Buku Lopatulika Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samuele; koma Samuele sanafike ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Saulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samuele; koma Samuele sanafike ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Saulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sauloyo adadikira masiku asanu ndi aŵiri, monga momwe adaanenera Samuele. Koma Samueleyo sadafike ku Giligala, ndipo anthu adayamba kumthaŵira Saulo uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Saulo anadikirira masiku asanu ndi awiri, monga mwa nthawi imene ananena Samueli. Koma Samueli sanabwere ku Giligala, ndipo anthu anayamba kumuthawa Sauli uja. |
Chomwecho Amasa anamuka kukaitana anthu a Yuda asonkhane; koma anachedwa, napitiriza nthawi imene idamuikira.
Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.