Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 12:4 - Buku Lopatulika

Ndipo iwo anati, Simunatinyenge, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina aliyense.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo iwo anati, Simunatinyenga, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina aliyense.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthuwo adati, “Simudatidyerere, kapena kutizunza, ngakhale kutenga kanthu kalikonse ka munthu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.”

Onani mutuwo



1 Samueli 12:4
6 Mawu Ofanana  

Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.


amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,


Demetrio, adamchitira umboni anthu onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.


Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.


Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wake ali mboni lero kuti simunapeze kanthu m'dzanja langa. Nati iwo, Iye ali mboni.