Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 10:2 - Buku Lopatulika

M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezeka; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezedwa; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

ukachoka pano lero, ukumana ndi anthu aŵiri ku manda a Rakele ku Zeliza m'dziko la Benjamini. Iwowo akuuza kuti abulu unkafuna aja adapezeka, ndiponso kuti bambo wako waleka kusamala za abuluwo, koma akudera nkhaŵa za iwe, akunena kuti, ‘Nditani ine m'mene mwana wanga sakuwonekamu?’

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’ ”

Onani mutuwo



1 Samueli 10:2
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa.


Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.


ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.


Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo.