Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 10:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’ ”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezeka; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezedwa; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 ukachoka pano lero, ukumana ndi anthu aŵiri ku manda a Rakele ku Zeliza m'dziko la Benjamini. Iwowo akuuza kuti abulu unkafuna aja adapezeka, ndiponso kuti bambo wako waleka kusamala za abuluwo, koma akudera nkhaŵa za iwe, akunena kuti, ‘Nditani ine m'mene mwana wanga sakuwonekamu?’

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 10:2
7 Mawu Ofanana  

Kenaka anachoka ku Beteli. Koma ali pafupi kufika ku Efurata nthawi yakuti Rakele aone mwana inakwana. Iye anavutika pobereka.


Pamene ndimabwerera kuchoka ku Parani, mwachisoni Rakele, amayi ako anamwalira mʼdziko la Kanaani, tikanali mʼnjira, mtunda wokafika ku Efurata ukanalipo. Ndipo ndinawayika kumeneko mʼmphepete mwa msewu wa ku Efurata” (amene ndi Betelehemu).


Yehova akuti, “Kulira kukumveka ku Rama, kulira kwakukulu, Rakele akulirira ana ake. Sakutonthozeka chifukwa ana akewo palibe.”


Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake. Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.


Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa