Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.
1 Samueli 10:18 - Buku Lopatulika nanena ndi ana a Israele, Atero Yehova, Mulungu wa Israele kuti, Ine ndinatulutsa Israele mu Ejipito, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aejipito, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena ndi ana a Israele, Atero Yehova, Mulungu wa Israele kuti, Ine ndinatulutsa Israele m'Ejipito, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aejipito, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adauza Aisraele onse kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akuti, ‘Ndidakutulutsani inu Aisraele ku dziko la Ejipito, ndipo ndidakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa mafumu onse amene ankakusautsani.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anawuza Aisraeli onse kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi kukupulumutsani mʼdzanja la Igupto ndi mʼdzanja la mafumu onse amene ankakuzunzani.’ |
Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.
Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.
Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse;
Pamene Yakobo anafika ku Ejipito, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anatulutsa makolo anu mu Ejipito, nawakhalitsa pamalo pano.