Eksodo 5:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Koma Farao anati, “Yehova ndani kuti ine ndimumvere ndi kulola Aisraeli kuti apite? Ine Yehova sindikumudziwa ndipo sindilola kuti Aisraeli apite.” Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Farao adayankha kuti, “Kodi Chautayo ndani kuti ine nkumvera zimenezo ndi kuŵalola Aisraele kuti apite? Chautayo sindimdziŵa, ndipo sindidzalola konse kuti Aisraele apite.” Onani mutuwo |
Choncho inu musalole kuti Hezekiya akunamizeni ndi kukusocheretsani motere. Musamukhulupirire, pakuti palibe mulungu wa mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse umene unatha kupulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa kapena mʼdzanja la makolo anga. Nanga bwanji Mulungu wanuyo, sadzatha kukupulumutsani kuchoka mʼdzanja langa!”
Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”