Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 4:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Zizindikiro zake ndi zazikulu, zozizwitsa zake ndi zamphamvu! Ufumu wake ndi wamuyaya; ulamuliro wake ndi wa mibadomibado.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 4:3
29 Mawu Ofanana  

“Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu, Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.


Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova! Munazipanga zonse mwanzeru, dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.


Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo, zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.


Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.


Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule.


Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.


Njira yanu inadutsa pa nyanja, njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu, ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.


Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndiye Mulungu.


Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi!


Yehova ndinu Mulungu wanga; ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu, pakuti mwachita zodabwitsa zimene munakonzekeratu kalekale mokhulupirika kwambiri.


Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.


Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya. Akakwiya, dziko limagwedezeka; anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.


Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu,


“Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya.


“ ‘Angelo oyera ndiwo akutsimikiza chilangochi. Tsono anthu adziwe kuti Mulungu Wammwambamwamba ali ndi mphamvu yolamulira maufumu onse, ndipo amawapereka kwa aliyense akumufuna, ngakhale munthu wamba kuti alamulire.’


Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.


Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ”


Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri! Ndani angazindikire maweruzidwe ake, ndipo njira zake angazitulukire ndani?


Kodi alipo mulungu amene anayeserapo kudzitengera mtundu wa anthu kuwachotsa mu mtundu unzake mwa mayesero, zizindikiro zozizwitsa, nkhondo, komanso mwa mphamvu zake zopanda malire, kapena mwa zochita zazikulu ndi zochititsa mantha, monga zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Igupto inu mukupenya?


Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.


Koma za Mwana wake akuti, “Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya, ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.


Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.


Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni.


Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa