Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo.