Danieli 2:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.” Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe. Onani mutuwo |
“Atumiki onse amfumu ndi anthu a zigawo za mfumu ankadziwa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akalowa ku bwalo lake la mʼkati mosayitanidwa ndi mfumu pali lamulo limodzi: lamuloli ndi lakuti aphedwe. Zimasintha pokhapokha ngati mfumu iloza munthuyo ndi ndodo yagolide kuti akhale ndi moyo. Koma papita masiku makumi atatu ndisanayitanidwe ndi mfumu.”
Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”