Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 10:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 10:1
28 Mawu Ofanana  

Popeza kuti malotowa aperekedwa kwa inu Mfumu kawiri, ndiye kuti Mulungu watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi posachedwapa.


Mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Peresiya, pofuna kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anakhudza mtima wa mfumu ya Peresiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse ndipo anazilemba:


Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.


Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.”


Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo.


Ndipo akuluakulu a Ayuda anapitiriza ntchito yomanga ija molimbikitsidwa ndi aneneri Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Anamaliza ntchito yomanga Nyumbayo, monga momwe Mulungu wa Israeli analamulira ndiponso potsata lamulo la Koresi, Dariyo ndi Aritasasita, mafumu a ku Perisiya.


Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27.


Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’ ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna; iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’ ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ”


Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.


Ndipo Danieli anali kumeneko mpaka chaka choyamba cha ufumu wa Koresi.


Mkulu wa nduna za mfumu anawapatsa mayina atsopano: Danieli anamutcha Belitesezara; Hananiya anamutcha Sadirake; Misaeli anamutcha Mesaki; ndi Azariya anamutcha Abedenego.


Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.”


“Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi.


Koma iweyo, Danieli, sungitsa mawuwa, umate bukuli kufikira nthawi ya chimaliziro. Anthu ambiri adzapita uku ndi uko ndipo nzeru zidzanka zikukulirakulira.”


Ndipo anandiyankha kuti, “Pita iwe Danieli, pakuti mawuwa ndi osungidwa ndi omatidwa kufikira nthawi ya chimaliziro.


Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.


Potsiriza, anabwera Danieli uja amatchedwa Belitesezara, potsata dzina la mulungu wanga, ndipo mzimu wa milungu yoyera uli mwa iye. Iyeyu ndinamufotokozera malotowo.


Munthu ameneyu dzina lake ndi Danieli, koma mfumu inamutcha Belitesezara ndipo ali ndi nzeru zapadera, ndi wodziwa ndi kuzindikira zinthu, ndiponso luso lakutanthauzira maloto, kufotokozera miyambi ndi kuthetsa mavuto osautsa. Muyitaneni Danieli, ndipo adzakuwuzani chomwe mawuwa akutanthauza.”


Pamenepo Danieli anayankha mfumu kuti, “Inu musunge mphatso zanuzo kwa inu nokha ndipo mupereke mphothoyo kwa wina aliyense. Komabe ine ndi kuwerengerani malembawa mfumu; ndikukuwuzani tanthauzo lake.


Choncho Danieli anapeza ufulu pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo ndi ulamuliro wa Koresi wa ku Perisiya.


Ndipo ndinamva mawu a munthu kuchokera mʼmbali mwa mtsinje wa Ulai akuyitana kuti, “Gabrieli, muwuze munthuyu tanthauzo la masomphenyawo.”


“Masomphenya okhudza madzulo ndi mmawa amene unawaona aja ndi woona, koma uwasunge masomphenyawa mwachinsinsi popeza ndi onena za masiku a mʼtsogolo kwambiri.”


Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”


Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa