Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 1:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda mʼdzanja lake, pamodzi ndi zina mwa zida zotumikira mʼNyumba ya Mulungu. Iye anazitenga napita nazo ku nyumba ya mulungu wake ku Babuloni ndi kuziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha mulungu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 1:2
30 Mawu Ofanana  

Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.


Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.


Pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anadzathira nkhondo dzikolo ndipo Yehoyakimu anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zitatu. Koma kenaka anasintha maganizo ake nawukira Nebukadinezara.


Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.


Nebukadinezara anatenganso zipangizo za ku Nyumba ya Yehova kupita nazo ku Babuloni ndipo anaziyika mʼnyumba ya Mulungu wake kumeneko.


Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake.


Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.


Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha, ndi Israeli kwa anthu akuba? Kodi si Yehova, amene ife tamuchimwirayu? Pakuti sanathe kutsatira njira zake; ndipo sanamvere malangizo ake.


Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni.


Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu.


Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni.


Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anathira nkhondo dziko lino, ife tinati, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithawe magulu ankhondo a Akasidi ndi Aaramu.’ Kotero ife takhala tikukhala mu Yerusalemu.”


“Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina, kweza mbendera ndipo ulengeze; usabise kanthu, koma uwawuze kuti, ‘Babuloni wagwa; mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi, nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha. Milungu yake yagwidwa ndi mantha ndipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’


Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni, ndidzamusanzitsa zimene anameza. Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye. Malinga a Babuloni agwa.


Choncho anabwera naye Danieli pamaso pa mfumu ndipo inati kwa iye, “Kodi ndiwe Danieli, mmodzi mwa akapolo omwe abambo anga mfumu anabwera nawo kuchoka ku Yuda?


“Inu mfumu, Mulungu Wammwambamwamba anapatsa abambo anu Nebukadinezara mphamvu ndi ukulu ndi ulemerero ndi ufumu.


Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake ndiponso kufukizira lubani khoka lake, popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.


Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”


Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000 kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse, Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa, Yehova akanapanda kuwataya?


Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse.


Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu.


Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu.


Kenaka anatenga Bokosi la Chipanganolo nabwera nalo ku nyumba ya Dagoni ndi kuliyika pambali pa Dagoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa