5 Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?
5 Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?
5 “Funsa anthu onse a m'dziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya ndi kulira pa mwezi wachisanu ndi pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri zaka makumi asanu ndi aŵiri zapitazi, kodi munkalemekezadi Ine pochita zimenezo?
5 “Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine?
Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babiloni adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmaakati, iwo ndi anthu ao omwe.
Koma kunali mwezi wachisanu ndi chiwiri anadza Ismaele mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yachifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Ababiloni okhala naye ku Mizipa.
Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritse ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi lubani.
Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.
Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa mu Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:
chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.
Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?
nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri?
Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.
Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.