Zekariya 1:21 - Buku Lopatulika21 Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Ine ndidafunsa kuti, ‘Kodi akudzachita chiyani?’ Iye adayankha kuti, ‘Mphamvu zijazi zidabalalitsa Yuda ndi Yerusalemu kotheratu, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woŵeramutsa mutu. Koma amisiri osulaŵa, abwera kudzaopsa ndi kudzaononga mphamvu za mitundu ya anthu imene idaagonjetsa dziko la Yuda, ndi kumwaza anthu ake.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Ndinafunsa kuti, “Amisiri a zitsulowa akudzachita chiyani?” Iye anayankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda kotero kuti panalibe wina amene akanalimbana nazo, koma amisiri a zitsulowa abwera kudzaziopseza ndi kugwetsa nyanga zimenezi za mitundu ya anthu amene analimbana ndi dziko la Yuda ndi kubalalitsa anthu ake.” Onani mutuwo |