Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 1:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono munthu amene anaima pa timitengo tazitsamba uja anayankha kuti, ‘Ameneŵa ndiwo amene Chauta waŵatuma kuti ayendere dziko lapansi.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pamenepo munthu amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu anafotokoza kuti, “Amenewa ndiwo amene Yehova wawatuma kuti ayendere dziko lonse lapansi.”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 1:10
13 Mawu Ofanana  

Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo.


Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula.


Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.


ndipo taonani, chozunguniza chantovu chotukulidwa: ndipo ichi ndi mkazi wokhala pakati pa efa.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa