Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 2:12 - Buku Lopatulika

12 Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Ngakhale tsopano, bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 2:12
39 Mawu Ofanana  

Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwo. Davide nati kwa Yehova, Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; koma tsopano Yehova muchotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinachita kopusa ndithu.


Tsono amtokoma anamuka ndi makalata ofuma kwa mfumu ndi akulu ake mwa Israele ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israele, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Israele, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asiriya.


pamenepo mumvere Inu mu Mwamba, nimukhululukire tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israele, mutawalangiza njira yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale cholowa chao.


Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka mu Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israele, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe chomwe ndikuchitireni.


Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;


Taonani, inu musala kudya kuti mukangane ndi kutsutsana ndi kukantha ndi nkhonya yoipa; inu simusala kudya tsiku lalero kuti mumveketse mau anu kumwamba.


Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.


Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yake yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukulu.


Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa.


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.


M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.


Ndiye Mkanani, m'dzanja lake muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa.


Israele, bwerera kunka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.


Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.


Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.


nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri?


Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?


Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.


komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.


Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.


Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.


Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.


Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele mu Mizipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa