Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 6:68 - Buku Lopatulika

68 Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

68 Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

68 Simoni Petro adati “Ambuye, nanga tingapitenso kwa yani? Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

68 Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:68
17 Mawu Ofanana  

Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.


Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.


Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Khristu.


Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu.


Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.


Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake lili moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula.


chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.


Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.


Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.


Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.


Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.


Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule mu Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.


Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa