Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 6:54 - Buku Lopatulika

54 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

54 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

54 Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

54 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:54
12 Mawu Ofanana  

Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.


koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.


Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira ali nao moyo wosatha.


Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.


Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.


Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa