Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 5:45 - Buku Lopatulika

45 Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Musayese kuti ndine amene ndidzakunenezeni kwa Atate, ai. Wodzakunenezani alipo. Ndi Mose yemwe uja amene inu mumamdalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 “Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 5:45
14 Mawu Ofanana  

Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.


Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.


Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha chifukwa ninji?


Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.


Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo;


Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa