Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 2:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati mu Kana wa mu Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Patapita masiku aŵiri, kunali ukwati ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko,

Onani mutuwo Koperani




Yohane 2:1
17 Mawu Ofanana  

Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino; Yehova amkomera mtima.


Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.


Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.


M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


M'mawa mwakenso analikuimirira Yohane ndi awiri a ophunzira ake;


M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.


Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake.


Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa mu Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala mu Kapernao.


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa