Yohane 19:11 - Buku Lopatulika11 Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Yesu adati, “Akadapanda kukupatsani mphamvu zimenezo Mulungu, sibwenzi mutakhala nazo konse mphamvu pa Ine. Nchifukwa chake amene wandipereka kwa inu ali ndi tchimo lalikulu koposa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Yesu anayankha kuti, “Inu simukanakhala ndi mphamvu pa Ine akanapanda kukupatsani kumwamba. Nʼchifukwa chake amene wandipereka Ine kwa inu ndiye wochimwa kwambiri.” Onani mutuwo |
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.
ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.