Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 16:21 - Buku Lopatulika

21 Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Pa nthaŵi yochira mai amavutika chifukwa nthaŵi yake yafika. Koma pamene wabadwa mwana, saganizakonso za kuzunzikako, chifukwa cha chimwemwe chakuti kunja kuno kwabadwa mwana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 16:21
18 Mawu Ofanana  

Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.


pakuti udzaiwala chisoni chako, udzachikumbukira ngati madzi opita.


Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana, akhale mai wokondwera ndi ana. Aleluya.


ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.


Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.


Mkazi asanamve zowawa, anabala mwana; kupweteka kwake kusanadze, anabala mwana wamwamuna.


Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.


Tsono ufuulitsa chifukwa ninji? Palibe mfumu mwa iwe kodi? Watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?


Pakuti kwalembedwa, Kondwera, chumba iwe wosabala; imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna.


Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa