Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 7:8 - Buku Lopatulika

8 Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 “Koma onani, inu mumakhulupirira mabodza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 7:8
14 Mawu Ofanana  

Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;


amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;


Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.


Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.


Ichi chidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a chinyengo cha mtima wao?


Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao achabe; koma Ine sindinatume iwo, sindinauze iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.


Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutume iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.


Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa.


Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa