Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 38:3 - Buku Lopatulika

3 Yehova atero, Mzindawu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yehova atero, Mudziwu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mzinda uno udzaperekedwadi kwa ankhondo a mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mzinda uno udzaperekedwa ndithu kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulande.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 38:3
7 Mawu Ofanana  

Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.


Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.


Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.


Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mzinda uno, abale anu amene sanatulukire pamodzi ndi inu kundende;


Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mzinda uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.


koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa