Yeremiya 38:2 - Buku Lopatulika2 Yehova atero, Iye wakukhala m'mzindawu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Yehova atero, Iye wakukhala m'mudziwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Chauta akunena kuti, “Aliyense amene atsalire mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Koma aliyense amene atuluke kukadzipereka kwa Ababiloni adzakhala moyo, adzapulumutsa moyo wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 “Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo. Onani mutuwo |