Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 3:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kuchuluka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la chipangano cha Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzachitanso konse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kuchuluka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la chipangano cha Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzachitanso konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Masiku amenewo mukadzachulukana m'dzikomo, anthu sadzalankhulanso za bokosi lachipangano la Chauta. Sadzaliganizira kapena kulikumbukira kapena kulisoŵa, ndipo sadzapanganso lina.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 3:16
24 Mawu Ofanana  

Wamng'ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m'nthawi yake.


Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.


Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.


Pa nthawi yomweyo adzatcha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.


Ndipo padzatuluka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzachulukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawachitiranso ulemu, sadzachepa.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.


Taonani, ndidzatenga iwo kudziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikulu lidzabwera kuno.


Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa.


Taonani, pokhala wamphumphu sunayenere ntchito iliyonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso ntchito iliyonse?


Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.


Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israele mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'lichero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.


Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika.


ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babiloni.


ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa