Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 27:4 - Buku Lopatulika

4 nuwauze iwo anene kwa ambuyao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Muzitero kwa ambuyanu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 nuwauze iwo anene kwa ambuyao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Muzitero kwa ambuyanu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Uŵauze kuti akadziŵitse atsogoleri ao kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuuza atsogoleriwo kuti:

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Uwapatse uthenga wokapereka kwa ambuye awo ndipo uwawuze kuti: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Mukawuze ambuye anu kuti:

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:4
8 Mawu Ofanana  

Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.


Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, chifukwa cha lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.


nuzitumize kwa mfumu ya Edomu, ndi kwa mfumu ya Mowabu, ndi kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kwa mfumu ya Tiro, ndi kwa mfumu ya Sidoni, ndi dzanja la amithenga amene afika ku Yerusalemu kwa Zedekiya mfumu ya Yuda;


Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.


Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Ndaika goli lachitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama zakuthengo.


Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa