Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:2 - Buku Lopatulika

2 Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 ndikalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu mau ake akuti, “Ndikukumbukira m'mene munkakhulupirikira pa unyamata wanu, m'mene poyamba paja munkandikondera monga amachitira mkwati wamkazi. Mudanditsata m'chipululu, m'dziko losabzalamo kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti, “ ‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako, mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi, mmene unkanditsata mʼchipululu muja; mʼdziko losadzalamo kanthu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:2
39 Mawu Ofanana  

Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.


Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.


Nzeru ifuula panja; imveketsa mau ake pabwalo;


Tulukani, ana aakazi inu a Ziyoni, mupenye Solomoni mfumu, ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake, ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake.


Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?


Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwachita.


nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;


Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati,


Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu?


Kodi kuyambira tsopano sudzafuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?


Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.


Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukire masiku a ubwana wako, muja unakhala wamaliseche ndi wausiwa, womvimvinizika m'mwazi wako.


Koma ndidzakumbukira Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.


Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.


Koma anachulukitsa zigololo zake, nakumbukira masiku a ubwana wake, muja anachita chigololo m'dziko la Ejipito.


ndipo anachita chigololo iwo mu Ejipito, anachita chigololo mu ubwana wao; pomwepo anthu anasindikiza mawere ao, pomweponso anakhudza nsonga za mawere za unamwali wao.


Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye mu unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao.


Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.


Ndipo ndidzampatsa minda yake yampesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.


Pakuti ndidzachotsa maina a Abaala m'kamwa mwake; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao.


Ndipo adzatsata omkonda koma osawagwira, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.


Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa.


Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.


Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.


Amene ali ndi makutu akumva, amve.


Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye.


Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.


Inde akonda mitundu ya anthu; opatulidwa ake onse ali m'dzanja mwanu; ndipo akhala pansi ku mapazi anu; yense adzalandirako mau anu.


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Koma ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa